fbpx

Mafunso

Ntchito za Zikomo Foundation zikuthandizanso dera la Likuni ku Lilongwe. Uku kudakhazikitsidwa Play Football Malawi academy yomwe ikuthandiza ana ndi a chinyamata. Timaona kuti tili ndi udindo waukulu kuthandiza anthu ovutika m’madera osiyanasiyana ngati ku Likuni.

 

Zikomo Foundation ndi Bungwe loyima palokha, silaboma ndipo cholinga chake si kupanga phindu. Likulu la Bungweli liri ku Switzerland. Timagwira ntchito zosintha miyoyo ya ana ndi a chinyamata angakhalenso akulu omwe. Pa dziko lapansi pali zambiri zimene siziyenda bwino, ndipo ife kudzera mu ntchito zathu tikusintha zina ndi zina mumagawo ochepa amene tikufikira. Bungwe la Zikomo Foundation lidalembedwa mu kaundula wa bungwe la misonkho ku Switzerland

Ndichiwerengero cha anthu choposera 16 Million, Malawi ndi dziko limodzi limene lili ndi chiwerengero cha anthu ochuluka mu Africa. Malawi ndi dziko limodzi losaukitsitsa pa dziko lapansi, anthu ochuluka sichikwanitsa kugwiritsa ntchito ndalama yokwanira 1 dollar pa tsiku malinga ndi kafukufuku wa 2005. Matenda a Aids ndi chilala ndizochuluka kwambiri mudzikoli. Malingana ndi a UNICEF, zaka zokhala ndi moyo zatsika kuchoka pa 45 kufika pa 39 kuyambiri chaka cha 2005. Chiwerengero chosadziwa kulemba ndi kuwerenga pakati pa a zibambo ndi 22.3 pa 100 alionse ndipo pakati pa azimayi ndi 36.7 %.

Thandizo lanu libweretsa kusintha kwakukulu. Ndimathandizo anu, mupangitsa kuti miyoyo yochuluka ya ana ndi achinyamata ku Malawi isinthe. Mathandizo apafupipafupi ndi okhazikika amathandiza kuti ntchito yathu isayime koma ikhazikike ndi kupita patsogolo.

Zikomo Foundation ikugwira ntchito mu maphunziro, za umoyo, chitukuko chosiyanasiyana. Ntchito zathu zakhazikika mu maphunzira a m’mera mpoyamba, ana a masiye, ndende ya a chinyamata, chipatala cha ana, zaulimi, ndi zina zachitukuko. Zikomo Foundation ikugwira ntchito yolimbana ndi umphawi pakati pa anthu.

Kupita ku Malawi kukuonetsani kufunikira konse kwa Bungweli. usiwa ku Malawi ndi waukulu, ndipo thandizo lililonse ndilofunikira kwambiri. Kudzera mu ntchito zathu tikuthandiza ana ochuluka ku Malawi. Anawa ndi tsogolo la dziko, chifukwa cha ichi, tikuika mphamvu zathu kutukula ana a ku Malawi.

Zikomo Foundation imapereka ntchito kwa eni ake a Malawi. Chitukuko china ndichoti tikuwalemba ntchito kuti athe kutukuka pamodzi ndi ma banja awo.

Zikomo Foundation imapereka mwayi wakugwira ntchito mothandizana. Timakonda kulumikizitsa anthu ndikuwathandizira kuti maluso awo apite patsogolo. muli olandiridwa kubwera kudzathandiza ntchito zathu kuti zipite patsogolo modzipereka.

Simon Holdener adayambitsa koyambilira Play Football Malawi, kenaka Zikomo Foundation. Izi zidachitika chifukwa cha mtima ofuna kuthandiza. Ndife oyamika chifkukwa cha zomwe takwaniritsa pa zaka 5 kuthandiza anthu ochuluka.

Zikomo Foundation ndi bungwe loyima palokha, lomwe silopangira phindu, likulu lake lili ku Switzerland. Ngati bungwe lothandiza, likugwira ntchito kumalawi kwambiri pakati pa a chinyamata ndi ana. Ife z Zikomo Foundation, sitimangoyang’anira zithu, koma timatengapo mbali pakubweretsa kusintha m’dziko.

Mukhoza kuthandiza Zikomo Foundation, mwina mukhoza kuthandiza mwana wa sukulu. Izi ndizokondweretsa pamene kudziwa kuti thandizo lanu likupereka kuthekera koti ana oposa 150 apeze mwayi wa ma phunziro. Timagwira ntchito ndi mabungwe ena kuti tikwanilitse masomphenya athu

Lembetsani pa Email: hello -at- zikomofoundation -dot- org, Social Medias, kapena lembetsani pa Kalata yathu

Pali kuthekera kungapo:

Kudzera pa Website

Ndondomeko ya ku Bank:

FCDA 14249761
NBS Bank Lilongwe Branch

Mwini Akaunti:

Zikomo Foundation
Pafupi ndi Bambino
Bwaila Street
Area 15/232

Kutumiza kuchokera ku Maiko ena:
BIC from Postfinance: POFICHBEXXX

Kapena tifunseni kalata yoperekera ndalama:
hello -at- zikomofoundation -dot- org

Lembetsani pa Email: hello -at- zikomofoundation -dot- org, Social Medias, kapena lembetsani pa Kalata yathu

Pali kuthekera kungapo:

Kudzera pa Website

Ndondomeko ya ku Bank:

FCDA 14249761
NBS Bank Lilongwe Branch

Mwini Akaunti:

Zikomo Foundation
Pafupi ndi Bambino
Bwaila Street
Area 15/232

Kutumiza kuchokera ku Maiko ena:
BIC from Postfinance: POFICHBEXXX

Kapena tifunseni kalata yoperekera ndalama:
hello -at- zikomofoundation -dot- org

Tikufunitsitsa kuti tisinthe  maphunziro ndi ophunzira ku Malawi. Zikomo Foundation ikuyika ndondomeko zimene zithandize kusintha maphunziro ku Malawi, tikumanga malo ophunziliramo abwino.

Mwana aliyense ali ndi ufulu wa maphunziro. kudzera mu maphunziro tsogolo a mwana limasulidwa. Paphunziro akupereka kuthekera kosiyanasiyan komwe kusinthe miyoyo.

 

Tikugwira ntchito yothandiza achinyamata amene ali m’ndende. Ndende ya Kachere ndi yakale, ndipo ikusunga anyamata ambiri omwe apalamula milandu yosiyanasiyana.

Malo ogona ndi osautsa ndipo chakudya chimene amalandira ndichosasililika komanso chosakwanira. Zikomo Foundation ikuthandiza kupereka chakudya, mankhwala, maphunziro ndi zina zimene zikubweretsa kusintha pa miyoyo yawo.

Kuyambira nthawi imene Zikomo Foundation idayamba kuthandiza anawa, pakhala ndikuoneka kusintha kwakukulu pakati pa anawa komanso bungwe losamalira anawa.

Crisis Nursery ikulandira thandizo la mwezi ndi mwezi (ndalama) zomwe zikuthandiza ana ndi omwe akuwayang’anira tsiku ndi tsiku.

Crisis Nursery imadalira kwambiri mathandizo ochokera kumadera osiyanasiyana.

Ndikovuta kwambiri kuti Boma likwaniritse kupereza zosowa zimene zilipo zambiri mu chipatala, maka ku ana, zomwe zina mwa izo ndi chakudya.

Chifukwa cha ichi Zikomo Foundation idatengapo mbali kuyamba kuthandiza wodi ya ana ku Kamuzu Central Hospital. Ana omwe ali ku chipatalaku ali ndi kusowa kwakukulu ndipo akufunikira thandizo lambiri. Mabanja ochuluka akulephera kuti akhoza kugula mankhwala komanso chakudya choyenelera chimene anawa akuchifuna.