Play Football Malawi
Bungwe la Play Football Malawi, limakhazikitsa malo a za masewero ndi maphuninziro ku Malawi, Cholinga chachikulu ndikuthandiza ana a ku Malawi powapatsa danga ndi kuwafikira mumagawo awa:
Maphunziro
Kudzera mu maphunzira, ana azindikira kuthekera kwao.
Mwana aliyense ali ndi ufulu wa maphunziro.
Chakudya
Chakudya chamagawo onse ndi chofunikira ku moyo wa thanzi wa mwana.
Masewero
Timaphunzira zambiri kudzera mu masewero.
Kupyolera ku masewero ampira wa miyendo tikufikira ana ochuluka.
Timalimbikitsa ana powathandiza kuti azindikire kuthekera kumene ali nako popanga zinthu zokhazikika zomwe zingasinthe miyoyo yawo, ya banja lawo komanso mudzi wawo. Kuti tikwaniritse izi, timatsindika pa kulumikizana ndi kugwilira ntchito limodzi ndi anzathu.
Dziwani zambiri poyang’ana pa tsamba lathu la intaneti: Play Football Malawi Website FAQ
Ku Maphunziro
Ku Malawi, si chachilendo kuona zithunzi za ana osachepera 100 atakhala pansi mkalasi lophunziliramo. Ambiri a anawa amakhalanso kuti alibe zipangizo zophunzilira ngati zolembera ndi polembapo. Ana ochulukanso alibe mwayi wa sukulu. Zikomo Foundation, ndi ma bungwe ena alowelerapo ndi kuyamba kumanga malo ophunzilirapo ndi kupereka zipangizo zophunzitsira ndi kuphunzilira.
Ndende ya a Chinyamata
Ndende ya a chinyamata nthawi zambiri imakhala yothithikana. Kusowekera kwa chakudya cha magulu, ukhondo ndi malo abwino ogona zimapangitsa kuti matenda achulukire ku maloku. a Zikomo Foundation timathandizira akayidi kuti apeze ma phunziro, chakudya choonjezera pa chomwe amadya, masewero olimbitsa thupi, komanso mankhwala osiyanasiyana.
Thandinzo kwa ana a masiye
Ku Malawi kuli ana amasiye ochuluka chifukwa cha kusoweka kwa umoyo wa thanzi, matenda a HIV/AIDS komanso kuchuluka kwa imfa za amayi panthawi ya kubereka kwao. a Crisis Nursery ali ndi nyumba imene amasungira ndikulelera ana amene mayi wawo wamwalira pa nthawi ya kubadwa kwao kufikira nthawi imene banja la kwao lingadzatenge udindo wa kuwalera. Zikomo Foundation imathandiza kumeneku m’magawo a ndalama, chakudya komanso zoseweretsa ana. Kulowelerapo kwathu, kumapereka kuthekera kwa Crisis Nursery kuti akwanitse ku samala ndi kulera ana ochuluka amene alibe mayi.
Thandizo ku chipatala cha ana
Chipatala cha Kamuzu Central ndicho chachikulu mu chigawo chapakati ku Malawi ndipo chimakhala chikuthandiza anthu ochuluka zomwe zimapangitsa kuti afune chithandizo chochuluka. mavuto alipo ochuluka ndipo Zikomo Foundation ikuthandiza magawo a chakudya, ukhondo ndi zina.
Thandizo kwa anthu osowa ndi okalamba
Umphawi wa ku ukalamba ndi waukulu kwambiri ku Malawi chifukwa kulibe ndondomeko zokhazikika zabwino zothandizira anthu omwe apuma pa ntchito kuchokera ku boma komanso mabungwe. Zikomo Foundation imagawa maphukusi athandizo mwezi uliwonse zomwe zimathandiza pa zofuna zawo za tsiku ndi tsiku ku Likuni kumene kuli sukulu yathu ya masewero a mpira wa miyendo.
Ntchito zina
Ngongole
Kupititsa patsogolo a malondo ang’onoang’ono timapangitsa kuti umoyo wa anthu utukuke ndi kupita patsogolo. Timathandiza anthu kukhazikitsa ndi kupititsa patsogolo malando awo powapatsa maphunziro komanso ngongole.
Ulimi
Alimi osachepera 750 million ku Africa alibe maphunziro ndi ukadaulo wa za ulimi zomwe zimapangitsa kuti asamapeze phindu mu ulimi wawo. Zikomo Foundation ikupanga ulimi wamakono molumikizana ndi alimi a m’midzi.
Zomangamanga
Zikomo Foundation ikulimbikitsa chitukuko cha zomangamanga. Nyumba zokhalamo ndi zogwilira ntchito ndi zokhumbika ku Malawi. Bungweli kudzera ku malo ake likhazikitsa nyumba, zokhalamo anthu komanso zogwilira ntchito.
-
« Ndikadzuka tsiku lililonse, ndimakhala okondwa kuti ife sitimangoganiza zochita zinthu zolondola koma kuti timachita zinthu zolondola »
Simon Holdener Oyambitsa bungwe
-
«Ndine okondwa kugwira ntchito ndi Zikomo Foundation. Masomphenya ake kuthandiza ana ndiogwira mtima. Ndili ndikufunitsitsa kuthandiza Africa, ndipo kugwira ntchito ndi ana ndiye tsogolo la Africa. »
James Phiri Wotsogolera ku Malawi
-
« Ndikuthandiza ntchito za Zikomo Foundation chifukwa ndimakhulupilira chitukuko cha mbali zonse. kungogawa zinthu zimakhala thandizo la lero lokha koma kusintha kaganizidwe ndi machitidwe komanso maphunziro ndi zinthu zokhazikika.»
Jürg Opprecht (†) wazamalonda
-
« Lero timakonda kukamba za vuto la kuchuluka kwa anthu othawa nkhondo ku maiko akwawo. Anthu mazanamaza a ku Africa amabwera kwathu kuno chifukwa cha mavuto amene ali m'dziko mwao. Kuti alimbikitsike ndi kusintha miyoyo yawo kuti akhoza kuchitapo kanthu za za m'maiko awo akufunika mabungwe ngati Zikomo Foundation.»
Marc Jost Khansala wa mzinda wa Bern
-
« Ndikukumbukira bwino kuti umoyo ndi khalidwe langa lidakonzeka chifukwa cha masewero a mpira. Ndaphunzira khalidwe labwino, kupilira ndikulimbana ndi kulephera. Ndiliokondwa ndi ntchito komanso njira zimene Zikomo Foundation ikutsata ndipo ndimakondwa kuthandiza ntchito zimenezi. »
Roman Josi Osewera Hoke NHL ochokera ku dziko lina
-
«Ine ndidabadwira ndi kukulira ku Africa. Ndikudziwa bwino m'mene masewera ampira amasinthira miyoyo. Kudzera mumasewero a mpira ndaphunzira kulimbikira ndikukwaniritsa zinthu zosiyanasiyana. Ndimtima wanga onse ndikuthandiza ntchito za Zikomo Foundation. »
Gilles Yapi Osewera Mpira kunja kwa dziko lake
-
« Kutukula anthu zikutanthauza kuwapatsa tsogolo ndi chiyembekezo »
Simon Holdener Oyambitsa bungwe
-
« Ndimadziwana bwino ndi otsogolera bungwe la Zikomo Foundation Simon Holdener. Bungweli likugwira ntchito yotamandika kwambiri yomwe ikubweretsa kusintha kosiyanasiyana m'miyoyo ya anthu aku Malawi. Ndikudziwa kuti ndili ndi udindo othandiza, nchifukwa chake ndikuthandiza bungweli.»
Mark Streit Osewera wakale wa hoke NHL
-
«Ndimathandiza Zikomo Foundation chifukwa kupyolera mu ntchito zawo ndikufikira anthu ochuluka. Pakuphunzitsa aphunzitsi, nde kuti ananso aphunzitsidwa bwino ndipo miyoyo yawo isintha kwakukulu »
Andreas Thür Wojambula zomangamanga
-
« Ndidali ndi mwayo okonza nawo mgonero wa Zikomo Foundation. Ndikhoza kufotokoza kuti ogwira ntchito olembedwa ndi ongodzipereka akugwira ntchito molimbika ndi kukhudzika konse ku Malawi. Ndikukhulupilira kuti Zikomo Foundation ipereka mwai ndikuthandiza kwakukula ana m'dziko la Malawi. "
Lukas Ninck Wogwira ntchito ku wailesi ya kanema
-
" Ndimasangalala kugwira ntchito ndi Zikomo Foundation chifukwa cha masomphenya ake. Ana ndi achinyamata ku Malawi apeza kuthekera kofikira ndi kupeza maphunziro apamwamba komanso kuphunzira luso la masewero a mpira la pamwamba. Zikomo Foundation ikupereka ndikugwira ntchito zapamwamba kwambiri. »
Davie Mpima Mkulu oyang'anira ndikuyendetsa masewero amphira ku Malawi